Sunday, January 17, 2010

M’gwirizano wadzetsa mtendere kuChiradzulu

Mfumu Likoswe yam’boma laChiradzulu idati kutha kwam’chitidwe odula ziwalo amayi komanso kuchepa kwaumbanda m’bolalo kwadza chifukwa cham’gwirizano omwe ulipo pakati paApolisi ndianthu am’midzi.
Boma laChiradzulu lidavutika kwambiri ndim’chitidwe waumbanda kumayambiliro azaka zam’ma2000, chinthu chomwe chidadzetsa mantha pakati paanthu am’bomalo.
M’chitidwewu udakula kwambiri m’dera lamfumu Likoswe, ndipo zimenezi zidakhumudwitsa mfumuyi, yomwe idadabwitsidwa ndichifukwa chomwe anthu ambandawa amkachitira zamtopolazi mdera lake.
Koma mfumu Likoswe yam’bolalo idati zonsezi tsopano ndimbiri yakale, ndipo anthu akugona mosayang’ana kukhomo, chinthu chomwe idati chatheka kamba kam’gwirizano wabwino pakati paApolisi ndianthu am’madera akumidzi kumeneko.
“Zinthu zidasintha tsopano ndipo kuno kuli mtendere tsopano. Zimenezi zatheka chifukwa cham’gwirizano wabwino omwe ulipo pakati paogwira ntchito zachitetezo ndianthu am’midzi,” idatero mfumu Likoswe.
Mfumuyi yathokoza anthu omwe amayang’anira ntchito zoonetsetsa kuti akuluakulu ogwira ntchito zolimbikitsa chitetezo akugwira ntchito limodzi ndianthu m’madera osiyanasiyana kamba kothandiza ndizida zosiyanasiyana monga zobvala pantchito, miyuni younikira usiku komanso psilili (mawezulo).
Akuluakulu olimbikitsa ntchitozi m’chigawo chakumwera sabata latha adapereka zovala anthu omwe akuthandizana ndiApolisi pantchito yobweretsa chitetezo, zinthu zomwe adati zithandiza kusiyanitsa pakati paanthuwa ndiena ongodziyendera usiku, mwina kamba kofuna kuchita zinthu zaumbanda.

No comments: