Sunday, May 2, 2010

Nkhani zaChichewa Sabata Ino

Kafukufuku athandiza kutukula miyoyo yaolumala
WOLEMBA RICHARD CHIROMBO
Bungwe laFedoma, lomwe ndimgwirizano wamabungwe oyang’anira anthu olumala m’dziko muno, lidati ambiri mwamavuto omwe anthu olumala akukumana nawo adza kamba kosowa kafukufuku weniweni wazosowa zaanthuwa.
Mneneri wabungweli, aPamela Juma, adati dziko laMalawi silidachitepo kafukufuku wachindunji wounika komanso kufukula zovuta zomwe anthu olumala akhala akukumana nazo, komanso momwe mavutowa angawathetsere.
AJuma adati masiku omwe anthu komanso mabungwe amkangoganiza zamavuto omwe anthu olumala amakumana nawo adatha, ndipo mpofunika kumachita kafukufuku othirira mang’ombe pazazinthu zomwe zikubwezeretsa m’mbuyo ntchito zachitukuko.
“Bungwe lathu lakhala likulandira madandaulo ochuluka okhudzana ndimavuto omwe anthu olumala akukumana nawo, ndipo tsopano taganiza zochita kafukufuku yemwe atiwunikire zamavutowa. Tagwirana Chanza ndimabungwe angapo, omwe achite kafukufuku m’maboma osiyanasiyana m’zigawo zones zadziko lino,”adatero aJuma.
Iwo adati ntchitoyi idzathandiza boma komanso mabungwe omwe siaboma kulimbikitsa ntchito zolimbikitsa kulemekeza ufulu waanthu olumala kumbali zones zachitukuko, kuphatikizapo kuncthito zaumoyo, maphunziro komanso zosamalira anthu.
Nduna yoona zaanthu olumala komanso okalamba, aReen Kachere, posachedwapa adapempha mabungwe aanthu olumala kuti adzinena zamavuto omwe adaululidwa ndikafukufuku, chinthu chomwe aKachere adati chidzathandiza boma kukonza ndondomeko zabwino zokhudza anthu olumala.
Boma, kudzera muunduna wazamalamulo, lakhala likuunika lamulo lokhudza maufulu aanthu olumala, komanso momwe angakhalire ndidanga lofanana ndianthu alunga pantchito zachitukuko, lomwe sadalipititse kunyumba yamalamulo kuti liyambe kugwira ntchito.

Alonjeza kupitiliza kumenyera ufulu anthu anse
WOLEMBA RICHARD CHIROMBO
Mkulu wabungwe laCentre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), lomwe lagwirana manja ndibungwe laCentre for Development of People (Cedep) polimbikitsa ntchito yoonetsetsa kuti anthu komanso boma akulemekeza ufulu waanthu onse, kuphatikizapo amuna kapena akazi ofuna kumakwatirana okhaokha, walonjeza kuti sasiya kulimbikitsa ntchitoyi angakhale anthu ena sakusangalatsidwa nazo.
Polankhula ndimtolankhani wathu sabata latha, Mkulu waCHRR, aUndule Mwakasungula, adati chitukuko sichingabwere m’dziko ngati boma komanso anthu akulemekeza ufulu wagulu limodzi laanthu, nthawi yomweyo mkumasala magulu amzika zina zadziko lomwelo.
AMwakasungula adapereka chitsanzo chankhani yaanthu aamuna kapena akazi omwe amapanga chisankho chokwatirana okhaokha, ndipo adati nawonso alindiufulu wawo Malingana ndipangano lomwe maiko onse apadziko lapansi adapanga pofuna kulemekeza ufulu waanthu onse mosayang’ana mtundu, mabadwidwe, kuchokera, chipembedzo ndizina.
“Ife sitisiya ntchito yolimbikitsa ufulu waanthu onse. Munthu aliyense ali ndiufulu ochita zones wasankha ndipo sibwino kuti boma kapena anthu adzipondereza ufulu woterewu. Maboma ali ndiufulu oteteza anthu ochepa kunkhaza zaanthu ambiri; nawonso mabungwe olimbikitsa ufulu waanthu alindiudindo owunikira anthu pazimenezi,” adatero aMwakasungula.
Anthu ambiri m’dziko muno asonyeza kudabwa ndimfundo zamabungwe ACHRR ndiCEDEP pankhani yaufulu waamuna kapena akazi kumakwatirana okhaokha, popeza akuti zimenezi sizikugwirizana ndichikhalidwe chachimalawi.
Palinso kusiya pakati pamabungwe omenyerera ufulu waanthu pankhaniyi, ndipo posachedwapa mkulu wabungwe loyang’anira ufulu waanthu laMalawi CARER aVera Chirwa adadzudzula m’chitidwewu ponena ati poti Mulungu adalenga mwamuna ndimkazi kuti achulukane.
“Amuna kapena akazi okhaokha sangachite zimenezi. Chodabwitsa n’chokuti amuna kapena akazi omwe amakwatirana okhaokha akufuna ana amatenga ana aanzawo, chomwe pachingerezi amati ‘dopushoni’,” adatero aChirwa.
Mtsogoleri wadziko lino, aBingu wa Mutharika, adalankhula koyamba pankhaniyi kumathero amwezi waEpulo, ndipo adati dziko laMalawi silingalole m’chitidwewu popeza ngochokera kwasatana.

No comments: