Sunday, December 1, 2013

UTHENGA WA PA TSIKU LOKUMBUKIRA MATENDA A EDZI PA DZIKO LONSE LAPANSI M’CHAKA CHA 2013- 2014 – KUCHOKERA KU NTHAMBI YA ZAUMOYO MU MPINGO WA KATOLIKA

Kufika pa mathero: - Pasakhalenso kufalikira kwa tsopano kwa kachirombo ka HIV
- Pasakhalenso kumwalira chifukwa cha matenda a Edzi
- Pasakhalenso kusalana chikwa cha kachilombo ka HIV kapena matenda a Edzi


Abale nd Alongo mwa Ambuye,

Landirani malonje lero patsiku la Mulungu loyamba mu nyengo ya Adiventi pamene mpingo ukuyamba chaka chatsopano cha chipembedzo, umene uli ulendo watsopano m’chikhulupiriro pamene tikukonzekera kubadwa kwa Ambuye athu Yesu Khristu pa Khrisimasi komanso kubweranso kwake kwachiwiri.

Leronso, pa 1 December, ndi tsiku lokumbukira matenda a Edzi padziko lonse lapansi. Ili ndi tsiku lofunikira ndi lopambana kwambiri chifukwa ndi pamene maboma, mabungwe okhudzana ndi za Edzi, mipingo komanso anthu osiyanasiyana amaunikira ndi kusinkhasinkha mozama za mliri wa Edzi. Apa ndi pamene tonse timagwirana manja pa nkhani yofufuza njira zothanirana ndi mliri wa Edzi.


Kufika pa mathero

Bungwe loyang’anira za kampeni yolimbana ndi matenda a Edzi linakhazikitsa mutu wakuti “kufika pa mathero” kuti tikhale tikuwusinkhssinkha kuyambira mchaka cha 2011 mpaka 2015. Mutu umenewu ukugwirizana ndi zimene bungwe la mgwirizano wa maiko onse pa dziko la pansi (United Nations) linagwirizano kuti pasakhalenso kufalikira kwa kachilombo ka HIV, pasakhalenso imfa zakudza chifukwa cha matenda a Edzi, ndipo pasakhalenso mchitidwe osalana chifukwa cha kachilombo ka HIV kapena matenda a Edzi.


Chifukwa chiyani tikuti kufika pa mathero?

Ntchito yomwe yakhala ikugwirka polimbana ndi mliri umenewu ikuwonetsa zipatso zabwino; ndipo izi ndi zimene zikutipatsa chilimbikitso ndi chiyembekezo kuti ndi zotheka kufika pa mathero a mliri umenewu.
 Malipoti akusonyeza kuti chiwerengero cha anthu otenga kachirombo ka HIV chinatsika nd 38% pakati pa 2007 ndi 2012; ndipo tikatenga akukuluakulu okhawokha, chiwerengerochi chinatsika nd 50%.
 Mchaka cha 2004, nambala ya anthu omwe ali ndi kachirombo inali 11.8% koma pofika 2010 inali itatsika kufikira 10.6%
 Pakali pano anthu pafupifupi 4 million anayezetsa magazi awo ndipo akudziwa momwe mthupi mwawo muliri. Izi zinatheka chifukwa m’dziko muno muli zipatala 569 zomwe zimapeleka uphungu ndi kuyeza magazi.
 Anthu opitirira 500,000 amene anapezeka ndi HIV anapatsidwa mwayi wolandira mnkhwala aulere, ndipo oposa 360000 ali moyobe ndipo akupitiriza kumwa makhwalawo.
 Chiwerengero cha anthu omwalira chifukwa cha matenda a Edzi chinatsika ndi 20% pakati pa chaka cha 2007 ndi 2010.

Ngakhale pali zipatso zabwino zoterezi, mliri wa matenda a Edzi udakali waukuli ndithu pakati pathu:
 Matenda a Edzi adakali nawo mu gulu la matenda odzetsa imfa za anthu ofunika pa chitukuko cha dziko. Mchaka chili chonse akumwalira anthu pafupifupi 46,000 chifukwa cha matenda a Edzi.
 Mwa ana amasiye onse amene ali mdzko muno, pafupifupi theka la iwo anataya makolo awo Kamba ka matenda a Edzi; ndipo mwa mabanja asanu aliwonse limodzi likulera ana a masiye.
 Pali anthu ambiri omwe anapezeka ndi kachirombo ka HIV koma sanapezebe mwayi woyamba nawo kulandira mankhwala otalikitsa myo awulele a ARV
 Kusowa kwa mankhawala mzipatala za mdziko muno kukuika pachiwopsezo moyo wa anthu amene ali ndi HIV kapena akudwala matenda a Edzi.
 Mchitidwe wosala anthu amene ali ndi kachirombo ka HIV kapena kudwala matenda a Edzi ukukulirakulira pakati pathu. Timamva nthawi zina kuti amayi kapena ana osiyidwa alandidwa katundu ndi achibale; kapena aMfumu akana kulemba dzina la wodwala matenda a Edzi pa mn'dandanda wa anthu woti alandire thandizo la chakudya kapena makuponi.

Zina mwa zinthu zobwezera m’mbuyo ntchito yolimbanirana ndi mliri wa Edzi zimachitika ngakhalenso m’tchalitchi mwathu momwe:

 Zimatheka munthu kumukaniza kutenga udindo wa pa tchalitchi chifukwa chakuti ali ndi kachirombo ka HIV kapena akudwala matenda a EDZI.
 Kusakhulupirika pakati anthu a pabanja komanso achinyamata kuchita mkhalidwe wogonana asanalowe m’banja.

Si onse mwa mavuto amene tatchulawa ali oyambitsa anthufe ayi; koma tikapanda kuchitapo kanthu tikuonetsa kulephera ndi kufooka kwathu, ndiponso kutayirira udindo wathu Akhristu. (1 Akorinto 12:27) Tikuyenera kufikira ena ndi mtima wachifundo ndi waubale makamaka kwa odwala amene ali gawo la thupi la Khristu. Paulo Woyera mu kalata yolembera aKhristu a ku Roma akuti “Muchite zimenezi chifukwa mukudziwa kuti yafika nthawi yakuti mudzuke kutulo. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera” (Aroma 13:11ff)


Tiyeni tichitepo kanthu

Tingathe kusintha zinthu momwe ziliri pano. Mutu wa tsiku lokumbukira matenda a Edziwu ukutitsimikizira kuti ndi zotheka kuthetseratu kufala kwa kachirombo ka HIV, kuthetseratu imfa zakuddza kaamba ka matenda a Edzi komanso kuthetseratu mchitidwe wosalana chifukwa cha kachirombo ka HIV kapena matenda a Edzi. Kuti zimenezi zitheke pakufunika kuti pamene anthu ena akuyamba mankhwala, pasakhalenso ena akutenga kachirombo ka HIV; anthu amene ali ndi kachilombo kapena akudwala, asamalidwe mokwanira; ndipo tisalole kuti mmodzi mwa wodwalawo amwalire chifukwa cha matend awoti angathe kuchiritsidwa. Anthu amene anapezeka ndi kachirombo ka HIV kapena akudwala matenda a Edzi akuyenera kupatsidwa ufulu ndi ulemu ngati munthu wina aliyense m’dziko muno.


a) Kuthetseratu kufalika kwa kachirombo ka HIV


Tikupempha:
 Anthu omwe ali pa banja kuti akhale wokhulupika kwa wina ndi mnzake komanso ayezetse magazi awo asanatenge pakati
 Achinyamata ndi onse amene sali pa banja kuti apewe mchitidwe ogonana mpaka nthawi yomwe adzamange banja
 Makolo, alangizi ndi mabungwe onse oyang’anira za achinyamata kuti awalangize mokwanira pofuna kuwathandiza kuti asasocheretsedwe ndi malangizo oipa kuchokera kwa anthu ena
 Akuluakulu amene ali ndi udindo wosungitsa chikhalidwe aonetsetse kuti akudzuzdula makhalidwe coipa achilendo amene akuyika miyoy ya anthu pa chiwopsezo chotenga kachirombo ka HIV.

b) Kuthetseratu imfa zakudza kaamba ka matenda a Edzi


Tikupempha:
 Boma ndi mabungwe othandiza boma awonetsetse kuti mankhwala aulere otalikitsa moyo akupezeka ndi kufikira wina aliyense amene anapezeka ndi kachirombo ka HIV
 Boma ndi mabungwe othandiza boma awonetsetse kuti anthu amene akudwala matenda a Edzi apeze zonse zowayenereza pa moyo wawo monga chakudya chopatsa thanzi ndi madzi abwino.
 Onse ogwira ntchito yosamalira odwala kuchipatala kapena kumudzi kuti agwire ntchito yawo mokhulupirika ndi mwachikondi.
 Akhristu onse ndi anthu onse akufuna kwabwino alimbike pantchito yosamalira ndi kuthandiza anthu amene ali ndi kachirombo ka HIV, wodwala matenda a Edzi, ndiponso wosiyidwa kamba ka Edzi.


c) Kuthetseratu mchitidwe wosalana


Tikupempha:
 Akhristu, mabungwe nd anthu onse akufuna kwabwino kuti apititse patsogolo ndi kuteteza ufulu wa anthu onse omwe ali ndi kachirombo ka HIV, wodwala matenda a Edzi komanso a masiye.
 Boma ndi onse okhudzidwa ndi ntchito yosamalira anthu kuti awonetsetse kuti awafikira mwapadera anthu amene ali ndi kachirombo ka HIV, wodwala matenda a Edzi komanso a massiye, pamene akugawa mathandizo wosiyanasiyana (monga makuponi a feteleza komanso chakudya nthawi ya njala)


Mau otsiriza

Khristu Mfumu ya Mtendere ndi Mfumu yachilungamo Yesaya 9:5-6) akubwera ndi uthenga wabwino kwa osauka ndi oponderezedwa. Khristu akutipatsa chiyembekezo ndi moyo watsopano: anthu amene anali mu m’dima adzaona kuwala kwakukulu (Yesaya 9:1). Tsono ngati atumiki a Khristu tiyeni tidzetse chiyembekezo, kuwala ndi moyo wochuluka kwa abale and alongo athu amene akuvutika ndi mliri wa Edziwu. Ngati timawakonda anzathu mowonadi sipangakhale mchitidwe wosalana, koma kuyesetsa kuwathandiza kuti akhale moyo wawo mosangala ndiponso kuti pasapekeze wina aliyense womwalira chifukwa chosowa chisamaliro. Tiyeni tichitepo kanhtu pamene tikuwona abale athu akutsata makhalidwe wowayika pachiwopsezo chotenga kachirombo ka HIV.



pasakhalenso kufalikira kwa kachilombo ka HIV
pasakhalenso imfa zakudza chifukwa cha matenda a Edzi
pasakhalenso mchitidwe osalana chifukwa cha HIV kapena Edzi

No comments: